1 Chronicles 16:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asafu ndiye amene anali mtsogoleri, ndipo omthandiza wake anali Zekariya, Yeiyele, Semiramoti, Yehiyele, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obededomu ndi Yeiyele. Ameneŵa ndiwo adasankhindwa kuti akhale oliza azeze ndi apangwe. Asafu ndiye amene anali woliza ziwaya zamalipenga,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asafu ndiye mkulu wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeiyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Matitiya, ndi Eliyabu, ndi Benaya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asafu ndiye mkuru wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Matitiya, ndi Eliabu, ndi Benaya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;