1 Chronicles 16:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo ndi limene Davide adayamba kulamula Asafu ndi abale ake kuti akhale oyang'anira nyimbo zothokoza Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ochita ndiwo Asafu ndi abale ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ocita ndiwo Asafu ndi abale ace.