1 Chronicles 17:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atayamba kukhazikika m'nyumba yachifumu, tsiku lina adauza mneneri Natani kuti, “Ine ndikukhala m'nyumba yachifumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, koma Bokosi lachipangano la Chauta likukhala m'hema.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pokhala Davide m'nyumba mwake, Davideyo anati kwa Natani mneneri, Taona, ndikhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la chipangano la Yehova likhala m'nsalu zotchinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pokhala Davide m'nyumba mwace, Davideyo anati kwa Natani mneneri, Taona, ndikhala ine m'nyumba yamikungudza, koma Gkasa la cipangano likhala m'nsaru zocinga.