1 Chronicles 17:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, monga m'mene ndidaachitira ndi Saulo kuti uloŵe ufumu ndiwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakhala atate wake, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamchotsera chifundo changa monga muja ndinachotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Ine sindidzasiya kumukonda monga ndinachitira ndi amene unalowa mʼmalo mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakhala atate wace, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamcotsera cifundo canga monga muja ndinacotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;