1 Chronicles 17:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndi mtundu uti pa dziko lapansi uli wofanafana ndi anthu anu Aisraele, amene Inu Mulungu mudaŵaombola kuti akhale anthu anu? Mudatchuka kwambiri poŵachitira zinthu zazikulu ndi zoopsa, ndiponso popirikitsa mitundu ina ya anthu pamene ankafika anthu anu, amene mudaŵaombola ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiwo ayani akunga anthu anu Israele, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikulu ndi zoopsa, pakupirikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Ejipito?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola, monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiwo ayani akunga anthu anu Israyeli, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikuru ndi zoopsa, pakupitikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Aigupto?