1 Chronicles 17:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho dzina lanu lidzakhala lomveka mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israele, ndiyedi Mulungu wao wa Israele!’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde likhazikike dzina lanu, likulitsidwe kosalekeza, ndi kuti, Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele; akhalira Israele Mulungu; ndi nyumba ya Davide mtumiki wanu ikhazikika pamaso panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kotero dzina lanu likhazikike ndi kukhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa woyangʼanira Israeli, ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde likhazikike dzina lanu, likulitsidwe kosalekeza, ndi kuti, Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israyeli; akhalira Israyeli Mulungu; ndi nyumba ya Davide mtumiki wanu ikhazikika pamaso panu.