1 Chronicles 17:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Konse kumene ndakhala ndikuyenda ndi Aisraele onse, kodi ndidaauzapo ndi mmodzi yemwe mwa aweruzi a Aisraele, amene ndidaŵalamula kuti azisunga anthu anga, kuti bwanji sudandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali ponse ndinayenda nao Aisraele onse ndinanena kodi mau ndi woweruza aliyense wa Israele, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense wa atsogoleri awo amene ndinamulamula kuweta anthu anga kuti, ‘Kodi nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali ponse ndinayenda nao Aisrayeli onse ndinanena kodi mau ndi woweruza ali yense wa Israyeli, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?