1 Chronicles 17:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzamveketsa dzina lako, kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndakhala ndi iwe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akulu okhala padziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndakhala ndi iwe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akuru okhala padziko.