1 Chronicles 18:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adatuma mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Tou kaŵirikaŵiri. Tsono adamtumizira Davide mphatso zamitundumitundu zopangidwa ndi golide, siliva ndi mkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anatumiza Hadoramu mwana wake kwa mfumu Davide, kumlonjera ndi kumdalitsa, popeza adayambana ndi Hadadezere, namkantha; pakuti Hadadezere adachita nkhondo ndi Tou; ndipo anali nazo zipangizo za mitundumitundu za golide ndi siliva ndi mkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anatumiza Hadoramu mwana wace kwa Davide, kumlankhula ndi kumdalitsa, popeza adayambana ndi Hadarezeri, namkantha; pakuti Hadarezeri adacita nkhondo ndi Tou; ndipo anali nazo zipangizo za mitundu mitundu za golidi ndi siliva ndi mkuwa.