1 Chronicles 18:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Davide adalanda Hadadezere magaleta 1,000, anthu a pa akavalo 7,000, ndi asilikali apansi 20,000. Atatero, Davide adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okoka magaleta, koma adasungako akavalo okwanira magaleta 100.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide analanda magaleta ake chikwi chimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magaleta, koma anasungako ofikira magaleta zana limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide analanda magareta ace cikwi cimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magareta, koma anasungako ofikira magareta zana limodzi.