1 Chronicles 18:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Davide adaika maboma a ankhondo ku Damasiko m'dziko la Siriya. Choncho Asiriyawo adasanduka otumikira Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Motero Chauta adampambanitsa Davideyo kulikonse kumene ankapita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anaika asilikali a boma m'Aramu wa Damasiko; ndi Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nazo mphatso. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anaika asilikari a boma m'Aramu wa Damasiko; ndi Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nazo mphatso, Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.