1 Chronicles 18:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera ku Tibati ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezere, Mfumu Davide adabwerako ndi mkuŵa wambiri. Ndi mkuŵa umenewo Solomoni adapanga chimbiya ndi nsanamira ndiponso ziŵiya zina za ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, midzi ya Hadadezere, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomoni anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera ku Teba ndi Kuni, mizinda ya Hadadezeri, Davide anatengako mkuwa wambiri umene Solomoni anapangira chimbiya, zipilala ndi zida zosiyanasiyana zamkuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, midzi ya Hadarezeri, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomo anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa.