1 Chronicles 19:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuona Yowabu tsono kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, anasankha amuna osankhika onse a Israele, nawanika ayambane ndi Aaramu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake; iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuona Yoabu tsono kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, anasankha amuna osankhika onse a Israyeli, nawanika ayambane ndi Aaramu.