1 Chronicles 19:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, mbale wa Yowabu, nakaloŵa mu mzinda. Pamenepo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wake, nalowa m'mudzi. Pamenepo Yowabu anadza ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai mʼbale wake ndi kulowa mu mzinda. Motero Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wace, nalowa m'mudzi. Pamenepo Yoabu anadza ku Yerusalemu.