1 Chronicles 19:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Asiriya ataona kuti Aisraele aŵagonjetsa, adatuma amithenga kuti abwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate, pamodzi ndi Sofaki mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona Aaramu kuti Israele anawakantha, anatumiza mithenga, natuluka nao Aaramu akukhala tsidya lija la mtsinjewo; ndi Sofaki kazembe wa khamu la Hadadezere anawatsogolera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, pamodzi ndi mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezeri, Sofaki akuwatsogolera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuona Aaramu kuti Israyeli anawakantha, anatumiza mithenga, naturuka nao Aaramu akukhala tsidya lija la mtsinjewo; ndi Sofaki kazembe wa khamu la Hadarezeri anawatsogolera.