1 Chronicles 19:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani nkukaŵapeza Asiriyawo. Adandanditsa ankhondo ake kuti amenyane nawo. Tsono pamene Davide ankandanditsa ankhondo ake mopenyana ndi Asiriya, iwoŵa adayamba kumenyana naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuuza Davide; namemeza iye Aisraele onse, naoloka Yordani, nawadzera, nanika nkhondo ayambane nao. Atandandalitsa nkhondo Davide kuyambana ndi Aaramu, anaponyana naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani. Iyeyo anapita kukakumana nawo ndipo anakhala mʼmizere yankhondo moyangʼanana ndipo iwo anamenyana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuuza Davide; namemeza iye Aisrayeli onse, naoloka Yordano, nawadzera, nanika nkhondo ayambane nao. Atandandalitsa nkhondo Davide kuyambana ndi Aaramu, anaponyana naye.