1 Chronicles 19:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo ankhondo a Davide adapha Asiriya okwera magaleta ankhondo okwanira 7,000, ndi ankhondo apansi okwanira 40,000. Adaphanso Sofaki mtsogoleri wa gulu lao lankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; ndipo Davide anapha Aaramu apamagaleta zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi anai; napha Sofaki kazembe wa khamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 7,000 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Iye anaphanso Sofaki, mtsogoleri wawo wankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israyeli; ndipo Davide anapha Aaramu apamagareta zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi anai; napha Sofaki kazembe wa khamulo.