1 Chronicles 19:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adati, “Ine ndidzamchitira zabwino Hanuni mwana wa Nahasi, pakuti inenso bambo wake ankandichitira zabwino.” Choncho Davide adatuma amithenga kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika kwa Hanuni, m'dziko la Aamoni, kuti akampepese.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati, Ndidzamchitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wake anandichitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wake. Pofika anyamata ake a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake. Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni kudzamupepesa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati, Ndidzamcitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wace anandicitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wace. Pofika anyamata ace a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,