1 Chronicles 19:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akalonga a Aamoni adauza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide watuma anthu odzakuthuzitsani mtima, ndiye kuti akulemekeza bambo wanu? Osati atumiki akewo abwera kwa inu kuti adzazinde dziko, ndipo kuti akalipenya, alilande?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kuchitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? Sakudzerani kodi anyamata ake kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi anthuwa sanawatumize kuti adzaone dziko lathu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kucitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? sakudzerani kodi anyamata ace kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?