1 Chronicles 19:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adamva za atumiki akewo, adatuma anthu kuti akakumane nawo, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye mudzabwere kuno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anamuka ena namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anachita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndevu zanu; zitamera mubwere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wina atafika ndi kufotokozera Davide za anthuwo, iye anatuma amithenga kukakumana nawo, chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anamuka ena, namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anacita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndebvu zanu; zitamera mubwere.