1 Chronicles 19:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, Hanuni ndi Aamoniwo adatumiza siliva wa makilogramu 34,000, kuti akalipirire magaleta ndiponso anthu a pa akavalo a ku Mesopotamiya, a ku Aramaaka ndi a ku Zoba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente chikwi chimodzi a siliva, kudzilembera magaleta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-Maaka, ndi ku Zoba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, Hanuni ndi Aamoni anatumiza siliva wolemera makilogalamu 34,000 kuti akalipirire magaleta ndi okwerapo ake a ku Mesopotamiya; Aramu-Maaka ndi Zoba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente cikwi cimodzi a siliva, kudzilembera magareta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-maaka, ndi ku Zoba.