1 Chronicles 19:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi gulu lake lankhondo. Amenewo adabwera nadzamanga zithando zankhondo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni adabwera kuchokera ku mizinda yao kudzamenya nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo anadzilembera magaleta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ake; nadza iwo, namanga misasa chakuno cha Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo analipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi ankhondo ake. Amenewa anabwera ndi kudzamanga misasa yawo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni anabwera kuchokera ku mizinda yawo ndipo anapita kukachita nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo anadzilembera magareta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ace; nadza iwo, namanga misasa cakuno ca Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.