1 Chronicles 19:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Aamoni adatuluka nandanda pa mizere yankhondo pa chipata cha mzinda. Koma mafumu amene adaadzawo anali paokha ku malo opanda mitengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo ku chipata cha mudzi, ndi mafumu adadzawo anali pa okha kuthengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene mafumu amene anabwera nawo anali kwa wokha, ku malo wopanda mitengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo ku cipata ca mudzi, ndi mafumu adadzawo anali pa okha kuthengo.