1 Chronicles 2:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Hezironi, ali wa zaka 60, adakakwatira mwana wa Makiri bambo wake wa Giliyadi. Ndipo mkaziyo adamubalira Segubu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pambuyo pake Hezironi analowa kwa mwana wamkazi wa Makiri atate wa Giliyadi, amene anamtenga akhale mkazi wake, pokhala wa zaka makumi asanu ndi limodzi mwamunayo; ndipo mkaziyo anambalira Segubu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pambuyo pace Hezroni analowa kwa mwana wamkazi wa Makiri atate wa Gileadi, amene anamtenga akhale mkazi wace, pokhala wa zaka makumi asanu ndi Gmodzi mwamunayo; ndipo mkaziyo anambalira Segubu.