1 Chronicles 2:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu a ku Gesuri ndi a ku Aramu adaŵalanda Havoti-Yairi, Kenati pamodzi ndi midzi yake yomwe, yonse pamodzi inalipo midzi 60. Onseŵa anali adzukulu a Makiri, bambo wake wa Giliyadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Gesuri ndi Aramu analanda midzi ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi milaga yake; ndiyo midzi makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Giliyadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Gesuri ndi Aramu analanda midzi ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi miraga yace; ndiyo midzi makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Gileadi.