1 Chronicles 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Yuda naŵa: Eri, Onani, ndi Sela. Ana atatu ameneŵa adamubalira ndi Batisuwa mkazi wa ku Kanani. Tsono Eri mwana wa Yuda anali wa makhalidwe oipa, choncho Chauta adamupha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana a Yuda anali awa: Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisua Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi iye anamupha.