1 Chronicles 2:55 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mabanjanso a alembi amene ankakhala ku Yabesi naŵa: Atirati, Asimeati ndi Asukati. Ameneŵa ndiwo Akeni amene adachokera kwa Hamati, kholo la banja la Rekabu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mabanja a alembi okhala ku Yabezi: Atirati, Asimeati, Asukati. Iwo ndiwo Akeni ofuma ku Hamati, kholo la nyumba ya Rekabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mabanja a alembi okhala ku Yabezi: Atirati, Asimeati, Asukati. Iwo ndiwo Akeni ofuma ku Hamati, kholo la nyumba ya Rekabu.