1 Chronicles 20:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Itayamba nthaŵi ya phukira chaka chotsatira, nthaŵi imene mafumu ankapita kukamenya nkhondo, Yowabu adatsogolera gulu lankhondo, nakaononga dziko la Aamoni, kenaka adapita kuti akazinge mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu. Tsono Yowabu adakantha mzinda wa Raba naugwetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Yowabu anatsogolera khamu lamphamvu, napasula dziko la ana a Amoni, nadza, naumangira misasa Raba. Koma Davide anakhala ku Yerusalemu. Ndipo Yowabu anakantha Raba, naupasula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Yowabu anatsogolera gulu la ankhondo. Iye anawononga Aamoni, kenaka anapita ku mzinda wa Raba ndipo anawuzungulira, koma Davide anatsala ku Yerusalemu. Yowabu anathira nkhondo mzinda wa Raba ndipo anawuwononga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pofikanso caka, nyengo yakuturuka mafumu, Yoabu anatsogolera khamu lamphamvu, napasula dziko la ana a Amoni, nadza, naumangira misasa Raba. Koma Davide anakhala ku Yerusalemu. Ndipo Yoabu anakantha Raba, naupasula.