1 Chronicles 20:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adaivula chisoti chagolide mfumu yao, ndipo atachiyesa, adapeza kuti chinkalemera makilogramu 5, ndipo pachisotipo panali mwala wamtengowapatali. Davide adachivala chisoticho, natenga zofunkha zochuluka mumzindamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumchotsa pamutu pake, napeza kulemera kwake talente wa golide; panalinso miyala ya mtengo wake pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, natulutsa zankhondo za m'mudzimo zambiri ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Ndipo Davide anavala chipewacho. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumcotsa pamutu pace, napeza kulemera kwace talente wa golidi; panalinso miyala ya mtengo wace pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, naturutsa zankhondo za m'mudzimo zambiri ndithu.