1 Chronicles 20:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵatulutsa anthu amumzindamo, nakaŵagwiritsa ntchito ndi masowo, zikumbiro zachitsulo ndi nkhwangwa. Umu ndimo m'mene Davide adachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni. Pambuyo pake Davideyo adabwerera ku Yerusalemu pamodzi ndi ankhondo onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natulutsanso anthu anali m'mwemo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi zipangizo zochekera zachitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka Davide pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naturutsanso anthu anali m'mwemo, nawaceka ndi mipeni ya mana mano, ndi zipangizo zocekera zacitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu.