1 Chronicles 20:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka padaukanso nkhondo ndi Afilisti. Tsono Elihanani, mwana wa Yairi, adapha Lami, mbale wa Goliyati Mgiti, amene thunthu la mkondo wake linali lalikulu ngati mtanda woombera nsalu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliyati Mgiti, amene luti la mkondo wake linanga mtanda woombera nsalu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nkhondo inanso ndi Afilisti, Elihanani mwana wa Yairi anapha Lahimi mʼbale wake wa Goliati Mgiti, amene mkondo wake unali ngati ndodo yowombera nsalu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panalinso nkhondo ndi Afgisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliati Mgiti, amene luti la mkondo wace linanga mtanda woombera nsaru.