1 Chronicles 20:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalinso nkhondo ku Gati kumene kunali munthu wina wamtali, wa zala zakumanja uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zakumwendonso uku zisanu nndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zonse pamodzi zala 24. Iyeyonso anali mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panalinso nkhondo ku Gati; kumeneko kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene zala zake za kumanja ndi kumapazi ndizo makumi awiri mphambu zinai; zisanu ndi chimodzi ku dzanja lililonse, ndi zisanu ndi chimodzi ku phazi lililonse; nayenso anabadwa mwa chimphonacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati, panali munthu wina wamtali kwambiri, wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panalinso nkhondo ku Gati; kumeneko kunali munthu wa msinkhu waukuru, amene zala zace za kumanja ndi kumapazi ndizo makumi awiri mphambu zinai; zisanu ndi cimodzi ku dzanja liri lonse, ndi zisanu ndi cimodzi ku phazi liri lonse; nayenso anabadwa mwa cimphonaco.