1 Chronicles 21:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kodi pabwere zaka zitatu za njala, kapena inu mukhale miyezi itatu akukukanthani adani anu namakukugonjetsani pa nkhondo, kapena pagwe mliri wa masiku atatu m'dzikomo pamene Chauta adzakukanthani ndi lupanga, ndipo mngelo wa Chauta adzawononga zinthu m'dziko lonse la Israele.’ Tsono tsimikizani choti ndikamuyankhe amene adanditumayo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israele. Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji Iye amene anandituma ine?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mʼdziko mukhale njala zaka zitatu, mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu, akukukanthani ndi lupanga la Yehova, kapena mʼdziko mukhale mliri kwa masiku atatu, mngelo wa Yehova akuwononga Israeli yense.’ Ndipo tsono ganizirani bwino chomwe ndikamuyankhe amene wandituma.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israyeli, Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji iye amene anandituma ine?