1 Chronicles 21:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Davide adauza Gadi kuti, “Ine pamenepa ine ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka ndigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde ndisagwe m'manja mwa anthu ayi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zake zichulukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ine andilange ndi Yehova, pakuti chifundo chake ndi chachikulu kwambiri; koma ndisalangidwe ndi anthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zace zicurukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu.