1 Chronicles 21:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Mulungu adamtumadi mngelo uja kukaononga Yerusalemu. Koma pamene ankati aziwononga kumene, Chauta adaona namva chisoni, osafunanso kuchita choipacho. Choncho adauza mngelo woonongayo kuti, “Iyai, basi tsopano! Kwakwanira, bweza dzanja lakolo.” Nthaŵi imeneyo nkuti mngelo wa Chauta uja ataima pa malo opunthira tirigu a Orinani Myebusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mulungu anatumiza mngelo kuti awononge Yerusalemu. Koma pamene mngeloyo amachita zimenezi, Yehova anaona ndipo anavutika mu mtima chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka coipaci; nati kwa mthenga wakuononga, Cakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi,