1 Chronicles 21:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adakweza maso ake naona mngelo wa Chautayo ataimirira pakati pa dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, m'manja mwake ali ndi lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Tsono Davide, pamodzi ndi akuluakulu omwe, atavala ziguduli, adadzigwetsa choŵerama pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anakweza maso ake ndipo anaona mngelo wa Yehova atayima pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, mʼdzanja lake muli lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Ndipo Davide ndi akuluakulu, atavala ziguduli, anadzigwetsa pansi chafufumimba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anakweza maso ace, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lace, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akuru obvala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.