1 Chronicles 21:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Davide adalankhula ndi Mulungu nati, “Kodi sindine amene ndidalamula kuti akaŵerenge anthu? Ndachimwa ndine, ndipo ndachita choipa. Koma nkhosa izi, kodi zachita chiyani? Inu Chauta Mulungu wanga, dzanja lanu likanthe ine pamodzi ndi banja la bambo wanga. Koma lisati likanthe anthu anuŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, linditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma lisatsutse anthu anu ndi kuwachitira mliri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anati kwa Mulungu, “Kodi si ine amene ndinalamula kuti ankhondo awerengedwe? Ine mʼbusa ndi amene ndachimwa, ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Inu Yehova Mulungu wanga, langani ineyo pamodzi ndi banja langa, koma musalole kuti mliriwu ukhale pa anthu anuwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndacimwa ndi kucita coipa ndithu; koma nkhosa izi zinacitanji? dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, Gnditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma Gsatsutse anthu anu ndi kuwacitira mliri.