1 Chronicles 21:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mfumu Davide adauza Orinani kuti, “Iyai, koma ndichita chogula ndi ndalama ndithu pa mtengo wake wathunthu. Sindingatenge chinthu chako kuti ndichipereke kwa Chauta, kupereka ngati nsembe yopsereza chinthu chimene sindidachigule.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, Iai, koma ndidzaligula pa mtengo wake wonse; pakuti sindidzatengera Yehova chili chako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mfumu Davide inayankha Arauna kuti, “Ayi, ine ndikuti ndipereka mtengo wathunthu. Sindingatenge chinthu chako ndi kuchipereka kwa Yehova, kapena kupereka nsembe imene sindinayigule.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, lai, koma ndidzaligula pa mtengo wace wonse; pakuti sindidzatengera Yehova ciri cako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wace.