1 Chronicles 21:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yowabu adati, “Chauta achulukitse pa chiwerengero anthu ake makumi khumi kupambana m'mene alirimu. Kodi anthu onseŵa mbuyanga mfumu si atumiki anu? Nanga chifukwa chiyani mbuyanga akufuna zimenezi? Chifukwa chiyani akufuna kuchimwitsa Aisraele?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu anayankha kuti, “Yehova achulukitse ankhondo ake kukhala miyandamiyanda. Mbuye wanga mfumu, kodi anthu onsewa sali pansi panu? Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwitsa Israeli?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Yoabu, Yehova aonjezere pa anthu ace monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? nanga afuniranji cinthuci mbuyanga, adzaparamulitsa Israyeli bwanji?