1 Chronicles 21:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapereka chiŵerengero cha anthu onse kwa Davide. Ku dziko lonse la Israele kunali anthu 1,100,000 otha kumenya nkhondo, ndipo ku Yuda kunali 470,000 otha kumenya nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraele onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa Davide: Mu Israeli monse munali anthu ankhondo 1,100,000 amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga, kuphatikizapo anthu 470,000 a fuko la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoabu anapereka kwa Davide ciwerengo ca anthu owerengedwa. Ndipo Aisrayeli onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga,