1 Chronicles 21:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Davide adayamba kupemphera kwa Mulungu, adati, “Ndachimwa kwambiri ine pazimene ndachitazi. Koma tsopano ndikukupemphani kuti mundikhululukire tchimo langa ine mtumiki wanu, popeza kuti ndachita zopusa kwambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Davide anati kwa Mulungu, Ndachimwa kwakukulu ndi kuchita chinthu ichi; koma tsopano, muchotse mphulupulu ya kapolo wanu, pakuti ndachita kopusa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Davide anati kwa Mulungu, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Davide anati kwa Mulungu, Ndacimwa kwakukuru ndi kucita cinthu ici; koma tsopano, mucotse mphulupulu ya kapolo wanu, pakuti ndacita kopusa ndithu.