1 Chronicles 22:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukadzamvera mosamala malamulo ndi malangizo amene Chauta adalamula Mose kuti auze Aisraele, ndiye kuti zinthu zidzakuyendera bwino. Khala wamphamvu, limba mtima, usati uziwopa, usatinso ude nkhaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo udzalemerera, ukasamalira kuchita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israele; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo udzapambana ngati udzamvera mosamala malangizo ndi malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kudzera mwa Mose. Khala wamphamvu ndi wolimba mtima. Usachite mantha kapena kutaya mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo udzalemerera, ukasamalira kucita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israyeli; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.