1 Chronicles 22:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Movutikira kwambiri ine ndaperekera Nyumba ya Chauta matani 3,400 a golide, matani 34,000 a siliva, ndiponso mkuŵa ndi chitsulo zosadziŵika kulemera kwake, poti zinali zochuluka kwambiri. Ndasonkhanitsanso matabwa ndi miyala. Pa zimenezi uwonjezeponso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golide, ndi matalente zikwizikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake, pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine movutikira kwambiri ndapereka ku Nyumba ya Mulungu matani 3,400 agolide, matani 34,000 asiliva, ndiponso mkuwa ndi chitsulo, matabwa ndi miyala. Ndipo iwe utha kuwonjezerapo pa zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golidi, ndi matalente zikwi zikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, osayesa kulemera kwace, pakuti zidacurukaeli; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.