1 Chronicles 22:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uli nawo anthu antchito ambirimbiri: amisiri a miyala, amisiri a matabwa, ndiponso anthu a nzeru zosiyanasiyana osaŵerengeka, aluso pa ntchito zao
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uli naonso antchito ochuluka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akuchita ntchito zilizonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe uli ndi antchito ambiri: osema miyala, amisiri a miyala, ndi amisiri a matabwa, komanso anthu ambiri aluso la ntchito zosiyanasiyana,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uli naonso anchito ocuruka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akucita nchito ziri zonse;