1 Chronicles 22:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ikani nzeru zanu ndi mtima wanu pa kutumikira Chauta Mulungu wanu. Muyambepo tsopano kumanga Nyumba ya Chauta kuti muikemo Bokosi lachipangano la Chauta ndiponso ziŵiya zonse zofunikira pa chipembedzo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono perekani mtima wanu ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu. Yambani kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti mubweretse Bokosi la Chipangano la Yehova ndi zinthu zopatulika za Mulungu mʼNyumba ya Mulungu imene idzamangidwa chifukwa cha dzina la Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la cipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, ku nyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.