1 Chronicles 22:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adaperekanso zitsulo zochuluka zopangira misumali ya zitseko zapamakomo ndi nsimbi zomangira. Adaperekanso mkuŵa wochuluka, wokanika kuuyesa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nakonzeratu Davide chitsulo chochuluka cha misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wochuluka wosauyesa kulemera kwake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapereka zitsulo zambiri zopangira misomali ya zitseko za pa zipata ndi zolumikiza zake. Anaperekanso mkuwa wochuluka wokanika kuwuyeza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nakonzeratu Davide citsulo cocuruka ca misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wocuruka wosauyesa kulemera kwace;