1 Chronicles 22:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide ankati, “Mwana wanga Solomoni akali wamng'ono, wosadziŵa zinthu, ndipo nyumba imene akudzamangira Chauta iyenera kukhala nyumba yaulemerero kwambiri, yomveka ndiponso yoyenera kuichitira ulemu anthu a ku maiko onse. Nchifukwa chake ine ndikuti ndikonzeretu zambiri.” Motero Davide adapezeratu zipangizo zambiri asanamwalire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anati, Solomoni mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikulu yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mochuluka asanamwalire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anati, “Mwana wanga Solomoni ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Koma nyumba yomwe timangire Yehova iyenera kukhala yaulemerero, yotchuka ndi yokongola pamaso pa anthu a mitundu yonse. Choncho ndikonzekeratu zambiri.” Motero Davide anayikonzekera kwambiri asanamwalire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anati, Solomo mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikuru yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mocuruka asanamwalire.