1 Chronicles 22:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta adandiwuza kuti, ‘Iwe udapha anthu ambiri ndipo udamenya nkhondo zikuluzikulu. Chifukwa cha zimenezi, sindiwe amene udzandimangire nyumba ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wochuluka, popeza wachita nkhondo zazikulu; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova anandiyankhula kuti, ‘Iwe wapha anthu ambiri ndiponso wachita nkhondo zambiri. Sumangira dzina langa nyumba chifukwa wapha anthu ambiri pa dziko lapansi pamaso panga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wocuruka, popeza wacita nkhondo zazikuru; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;