1 Chronicles 22:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzabereka mwana wamwamuna. Iyeyo adzakhala munthu wamtendere. Ine ndidzamkhalitsa mwamtendere pakati pa adani ake onse omzungulira. Dzina lake adzatchedwa Solomoni, popeza kuti ndidzabweretsa bata ndi mtendere m'dziko lonse la Israele pa moyo wake wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phee; ndipo ndidzampumulitsira adani ake onse pozungulirapo, pakuti dzina lake lidzakhala Solomoni; ndipo ndidzapatsa Israele mtendere ndi bata masiku ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma udzabala mwana wamwamuna amene adzakhala munthu wamtendere ndi wabata ndipo ndidzamupatsa mpumulo kuchokera kwa adani ake onse a mbali zonse. Dzina lake adzatchedwa Solomoni ndipo Ine ndidzapereka mtendere ndi bata kwa Israeli pa nthawi ya ulamuliro wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phe; ndipo nelidzampumulitsira adani ace onse pozungulirapo, pakuti dzina lace lidzakhala Solomo; ndipo ndidzapatsa Israyeli mtendere ndi bata masiku ace;