1 Chronicles 23:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yahati anali mtsogoleri, ndipo Ziza anali wachiŵiri wake. Koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri, nchifukwa chake adaŵaŵerengera ngati makolo a banja limodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wamkulu wa iwo ndi Yahati, mnzake ndi Ziza; koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri, potero anakhala nyumba ya kholo yowerengedwa pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wamkuru wa iwo ndi Yahati, mnzace ndi Ziza; koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri, potero anakhala nyumba ya kholo yowerengedwa pamodzi.